Ku Ziyoni komanso m’banja lathu, kumvetsetsa chifukwa chimene munthu amachita zinthu mwanjira inayake kumatha kubweretsa chifundo, koma osadziwa chifukwa chake, titha kuwamvetsa molakwika, kukwiya, ndipo pamapeto pake timakhala adani.
Ndicho chifukwa Mulungu anatsindika kufunika kumvetsetsa ndi kuganizira wina ndi mzake ndipo anatsindika “kukonda wina ndi mzake” monga chiphunzitso chofunika cha pangano latsopano.
Mamembala a Mpingo wa Mulungu amaganizira za kuvutika, kupweteka, manyazi, ndi kunyozedwa komwe Atate ndi Amai anapirira chifukwa cha iwo, kutaya umunthu wawo wakale omwe ankakhala mwa iwo okha, ndikuyesetsa kukhala ndi umunthu watsopano omwe amaganizirana wina ndi mnzake, kudzipereka kwa wina ndi mzake, ndikuchita mwakhama chikondi.
Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye. . . . Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake. 1 Yohane 4: 16-21
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi