Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, anabwera kudziko lapansi ili, anapachikidwa, ndipo anapirira kusekedwa, chitonzo, ndi kuzunzidwa kwa anthu osawerengeka. Komabe, anapirira zonsezi mwakachetechete kuti apeze anthu ake oona, kutetedzera machimo awo onse, ndi kuwapulumutsa.
Mu ndongosolo la kupulumutsa ana akumwamba, Yesu pa kubwera Kwake koyamba, Khristu Ahnsahnghong pa kubwera Kwake kwachiwiri, ndi Amai Akumwamba Yerusalemu onse anabwera ku dziko lino lapansi m'thupi. Malinga ndi ulosi, njirayi mosalephera imaphatikizapo masiku achisoni, kutsatiridwa ndi masiku achimwemwe pamene ulemerero umalandiridwa. Mogwirizana ndi lonjezo ili, ulemerero wa Mulungu Amai, amene tsopano akutsogolera Mpingo wa Mulungu, ukuwululidwa padziko lonse lapansi.
Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala? Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu. Yohane 10:32-33
Dzuwa lako silidzalowanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha. Yesaya 60:20
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA 
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi